Chichewa 1. Buku la ophunzira la Sitandade
 9789996044991

  • Author / Uploaded
  • coll.

Citation preview

Malawi Primary Education

Chichewa Buku la ophunzira la Sitandade

1

Malawi Institute of Education

Produced and printed with support from

Adakonza ndi kusindikiza ndi a Malawi Institute of Education PO Box 50 Domasi Zomba Malawi Email: [email protected] Website: www.mie.edu.mw

© Malawi Institute of Education, 2016

Zonse za m’bukumu n’zosati munthu akopere mu njira ina iliyonse popanda chilolezo. N’zosatinso munthu achitire malonda mpang’ono pomwe. Komabe ngati munthu afuna kugwira ntchito ya za maphunziro ndi bukuli, ayambe wapempha ndi kulandira chilolezo kuchokera kwa eni ake omwe adalisindikiza. Kusindikiza koyamba 2016 ISBN 978-99960-44-99-1

Olemba Foster Gama : Malawi Institute of Education Frackson Manyamba : Malawi Institute of Education Jeremiah Kamkuza : Department of Inspectorate and Advisory Services Lizinet Daka : Department of Basic Education Rabson Madi : Department of Teacher Education Ivy Nthara : Domasi College of Education Wisdom Nkhoma : Domasi College of Education Ndamyo Mwanyongo : Kasungu Teachers' College Mordky Kapesa : Lilongwe Teachers' College Esther Chenjezi : Lilongwe Teachers' College Nicholas Kalinde : Machinga Teachers' College Jordan Namondwe : Chiradzulu Teachers' College Rex Chasweka : Blantyre Teachers' College Elias Chilenje : Phalombe Teachers' College Laston Mkhaya : Montfort Special Needs College Ethel Lozani : Mbandanga Primary School Catherine Mphimbya : Chankharamu Primary School Loya Chigolong'ondo : Waya Primary School

Kuthokoza A Unduna wa za Maphunziro, Sayansi ndi Umisiri pamodzi ndi a Malawi Institute of Education akuthokoza onse omwe adatengapo gawo m'njira zosiyanasiyana kuyambira polemba bukuli kufika polisindikiza. Iwowa akuthokozanso kwakukulu bungwe la United States Agency for International Development (USAID) ndi Department for International Development (DFID) pothandiza ndi ndalama komanso upangiri kuti buku la ophunzirali lilembedwe, liunikidwe ndi kusindikizidwa mogwirizana ndi Mulingo wa boma wowunikira maphunziro m'sukulu (National Education Standards) komanso Ndondomeko ya boma yokhudza kuwerenga m'sukulu (National Reading Strategy). Iwo akuthokozanso anthu onse omwe adaunikanso bukuli ndi kupereka upangiri osiyanasiyana.

Okonza Akonzi : Ojambula zithunzi : Wotayipa : Woyala mawu ndi zithunzi : Mkonzi Wamkulu :

Max J Iphani ndi Peter Ngunga Heath Kathewera Thabu Phiri ndi Lucy Chisambi Sanderson Ndovi Max J Iphani

Zamkatimu

Kuthokoza................................................ v Mutu 1 Malonje ndi zithunzi................... 1 Mutu 2 a n............................................. 5 Mutu 3 i m............................................. 7 Mutu 4 u k............................................. 9 Mutu 5 o l.............................................. 13 Mutu 6 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 17 Mutu 7 e w............................................ 21 Mutu 8 t d............................................. 25 Mutu 9 s p............................................. 29 Mutu 10 nd ch......................................... 33 Mutu 11 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 37 Mutu 12 y b............................................. 41 Mutu 13 z g............................................. 45 Mutu 14 r f.............................................. 49 Mutu 15 h j.............................................. 53 Mutu 16 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 57 Mutu 17 v dz........................................... 61 Mutu 18 mw nz........................................ 65 Mutu 19 kw ts......................................... 69

Mutu 20 th mb......................................... 73 Mutu 21 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 77 Mutu 22 kh ng......................................... 81 Mutu 23 ns mp........................................ 85 Mutu 24 nj ny.......................................... 89 Mutu 25 bw mt........................................ 93 Mutu 26 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 97 Mutu 27 ph ng'........................................ 101 Mutu 28 dw ps......................................... 105 Mutu 29 bz fw......................................... 109 Mutu 30 gw ml......................................... 113 Mutu 31 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 117

Mutu 32 mv dy........................................ 121 Mutu 33 ms sw........................................ 125 Mutu 34 mk mz........................................ 129 Mutu 35 Kubwereza ndi kuyesa ophunzira. 133

Mutu 1 Malonje ndi zithunzi

Mutu 1 Malonje ndi zithunzi

1

2

Mutu 1 Malonje ndi zithunzi

Mutu 1 Malonje ndi zithunzi

3

4

Mutu 2

a A

aA

nN

Mutu 2

a A

nN

nN

na ana

5

6

Mutu 3

i I

mM

a n

Mutu 3

i I

mM

na

mM

iI

ma mi amama

anama

ni

aima

ana ina

Ana anama. Amama aima. 7

8

Mutu 4

ma

u U

kK

Mutu 4

u U

kK

na

uU nu

mu

anu

umu

uma

una

nanu

Ana aima. Ana aima umu. Inu imani umu.

9

10

Mutu 4

u U

ma

na

kK

Mutu 4

u U

kK

ni

kK ku

ka

ki

kana

uku

ukani

kumana 11

uka

Ana inu ukani. Amama akumana nanu. 12

Mutu 5

na

lL

o O ni

Mutu 5

lL

o O

ka

oO ko

no

mo

onani aona moni

Moni ana inu.

mono koka

Ana aona amama. Amama akukoka mono.

13

14

Mutu 5

lL

o O

mo

mu

Mutu 5

lL

o O

ni

lL la

li

lo

lu Onani luni.

lumo

lamulo

lima

luni 15

lola

Ikani luni umu. Ana aika luni. 16

Mutu 6 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oyimira zinthu izi.

Mutu 6 3

Fananitsani lembo laling'ono ndi lalikulu mu mabokosi otsatirawa.

a n i m 4 2

Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu bokosi ili.

m o n u k a l i 17

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

M N A I

u k o l

O U K L

Werengani maphatikizo otsatirawa.

ma ka mu ni lo

ni nu la ko mi

mi mo ki lu na 18

na li no ma ku

Mutu 6 5

6

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani mawu otsatirawa.

ana

ina

mana

amama

umu

uku

anu

inu

lula

nola

kana

moni

koka

luni

ukani

kumana

Werengani ziganizo zotsatirazi.

Ana inu imani. Onani mono uko. Amama akukoka mono.

19

Mutu 6

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Ntchito yowonjezera

Lozani maphatikizo ofanana kuchokera ku A kupita ku B. Chitsanzo A 1 la

B 1 mi

2 mi

2 la

1 2 3 4 5

A ko no ma lu ni

B 1 2 3 4 5 20

ni lu ko no ma

Mutu 7

ku

e E li

wW

Mutu 7

e E

wW

ma

eE ne

me

ke

limene

lima

mema

ena

21

le leka

Melina alema. Melina aleka kulima. Amema ana ena kulima.

22

Mutu 7

lu

e E

Mutu 7

wW

ka

e E

wW

ko

wW wi

wo

we

wa

wu

wina

lowa

maluwa

owala

wauka

wako

23

Onani maluwa. Onani maluwa owala. Maluwa ena awauka. 24

Mutu 8

t T

ke

Mutu 8

dD

wa

t T

dD

li

tT te

tu

ta

atate

uta

tiana

tituta

25

to

ti

tomato

Atate alima tomato. Tiana tituta tomato. Kenaka tiana titula tomato.

26

Mutu 8

ku

t T la

Mutu 8

dD

t T

dD

wa

dD de

du

da

do

di Duku la Dola.

duku

lada

dala

adalowa

27

akudoda

Duku la Dola lada. Dola akututa tomato.

28

Mutu 9

ku

s S lu

Mutu 9

pP

s S

pP

wo

sS se

sa

so

su

si Ana akusesa.

sema sukulu sesa kusesa

29

seka

Amama asesa nawo. Ana ena akuseka.

30

Mutu 9

ta

s S ko

Mutu 9

pP

s S

pP

su

pP pi

pu

po

pa

poto

pita

popita

makope

pe

puma

Ana akupita kusukulu. Popita atola makope. Makope anali a ana ena.

31

32

nd

Mutu 10

do

wo

ch

Mutu 10

nd

ch

lu

nd nde ndo ndi ndu nda ndalama

ndulu

ndodo

ndiwo

33

ndolo

Atate ali ndi ndolo. Amama amakonda ndolo. Ana nawo amakonda ndolo. 34

Mutu 10

le

nd

pa

ch

Mutu 10

nd

ch

ke

ch cho cha chu chi che chule chake

chipatala chala

35

chatupa

Chala cha Chisomo chatupa. Chalachi chachita katulutulu. Mawa apita kuchipatala.

36

Mutu 11 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oimira zinthu izi.

Mutu 11 3

Fananitsani lembo laling'ono ndi lalikulu mu mabokosi otsatirawa.

e w t 4 2

Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu bokosi ili.

t p d ch nd w s e 37

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

W T E

s p d

p d s

Werengani maphatikizo otsatirawa.

wa do se chu pi

to

de wi ta pu wo sa di te ndu 38

wu we cha ndo si

ti du ndi pe cho

Mutu 11 5

6

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

7

Werengani mawu otsatirawa.

leka

wina

duku

atate

kulima

tituta

ndolo

sema

pita

chule

popita

kusesa

se

ko

chu

Atate alima tomato. Tomato wina ndi owola.

la da

wa ndo

to

Werengani ziganizo zotsatirazi.

B

po do

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Onani tomato.

Pangani mawu polumikiza maphatikizo a mu A ndi mu B. A

Mutu 11

sa

to

wa

le ta

si 39

40

Mutu 12

y Y

nda

wa

Mutu 12

bB

y Y

bB

pa

yY yi

ya

yu

yala

yalula

yanika

yoyola

yo waya

ye Amayi ayala pepala. Papepala ayanikapo usipa. Yamikani amakonda usipa.

41

42

Mutu 12

lo

y Y to

Mutu 12

bB lu

y Y

bB

wa

bB bo

bi

ba

bu

be Onani bowa.

botolo

bulu

bowa

waba

43

kuba

Bowawu ndi utale. Aika bowa mu beseni.

44

Mutu 13

sa

z Z ndo

Mutu 13

gG we

to

z Z

gG

wa

zZ zi

zo

za

zu

ze Ziweto zili kudondo.

zolusa

ziweto

izo

zina 45

zasowa

Izo zili chete kudondo. Ziweto zina zasowa. 46

Mutu 13

yo

z Z yi

Mutu 13

gG

nda

zi

gi

ge

z Z

gG

gG gu

go

ga Apa pali galimoto.

galu

galimoto

gunda gona 47

magazi

Galimotoyi yagunda galu. Galuyo samaona poti anagona. 48

Mutu 14

ka

r R

fF

wi

li

si

Mutu 14

r R

fF

rR re

ru

ro

awiri

sirira

lero

lirira

49

ri lira

ra Onani ana awiri akulira. Amayi aona ana akulira. Ana akulirira amama awo.

50

Mutu 14

r R

Mutu 14

fF

r R

fF

ga si ku

fF fi

fa

fu

fulu

fisi

funa

ife 51

fe fanana

fo Fisi akulira. Fisi amafuna kuba ziweto. Agalu ofanana akuuwa fisi.

52

Mutu 15

bu

h H

Mutu 15

jJ

wu

h H

jJ

gu

hH hu

ha

he

hamala

hema

mahewu

hutala 53

hi

ho

habu

Onani habu ndi hamala. Atate agula habu ndi hamala. Aika habu ndi hamala mu hema. 54

h H

Mutu 15

la

zi

Mutu 15

jJ

h H

jJ

si

jJ ji

ju

ja

jekete

juzi

jowa

Juni

55

je jasi

jo Kuno kumazizira mu Juni. Juzi la Joni ndi lakuda. Jekete la amayi ndi loyera. Jasi la atate ndi lobiriwira. 56

Mutu 16 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oimira zinthu izi.

Mutu 16 3

Fananitsani lembo laling'ono ndi lalikulu mu mabokosi otsatirawa.

y b z g 4 2

Tchulani liwu la lembo lililonse kuchokera mu bokosi ili.

g f y

j

r 57

b h z

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

B G Y Z

r f h j

H F J R

Werengani maphatikizo otsatirawa.

yi ba re fu ro

be zo zu ge fo ha zi jo ja hi 58

ga yo ju ra fe

yu gi bo he ya

Mutu 16 5

6

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani mawu otsatirawa.

yala

zina

galu

botolo

yanika

zolusa

lero

fula

habu

pilira

fanana

mahewu

Werengani ziganizo zotsatirazi.

Tadala waona chona. Chona akujowa.

Mutu 16 7

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Ikani mawu oyenera mu mipata ya ziganizo izi.

1 Galu waluma __________. (beru, chala) 2 Ana achapa____________. (majuzi, chete) 3 Gogodani kuti __________ . (mulowe, muone) 4 _________ la amama ndi lakuda. (Hema, Jekete)

Akufuna kugona pa tebulo.

59

60

Mutu 17

go

v V me

Mutu 17

dz ra

chi

vi

ve

v V

dz

vV vu

vo

vala

velo

vuka

vomera

61

vula

va Joni anavala chipewa. Wavula ataona agogo. Kuvula chipewa ndi ulemu. Agogo ake sanavale chipewa. 62

v V

Mutu 17

te

ra

lo

dz

Mutu 17

v V

dz

re

dz dze dzu dza dzi dzo madzi

mudzi

dzulo

dzana 63

dzira

Amayi atereka madzi pamoto. Aikamo dzira limodzi. Madzulo kuli luni ndi mazira. Dzana kudali usipa wouma. 64

Mutu 18

se

mw zi

ke

nz

Mutu 18

mw

nz

no

mw mwi

mwa

mwana

mwala

mwake

mwano 65

mwe mwezi

Lero mwezi wawala. Mwana wina akuloza mwezi. Wina ali pa mwala. Mwezi ukawala ana amasewera. 66

Mutu 18

mw

mwa

ru

Mutu 18

nz ze

mw

nz

ye

nz nzi nzo nza nzu nze nzama konza

wanzeru zunza

67

nzika

Melifa ndi wanzeru. Iye amakonza galimoto. Poweruka amagula nzama. Nzama zimakoma zedi. 68

Mutu 19

chu

kw

ts

sa

nu

wo

Mutu 19

kw

ts

lu

kw kwe

kwi

kwa

kwawa

kwawo

kwera

kwina

69

kwanu

Awa ndi ana akwanu. Iwo akukwera chulu mokwawa. Chuluchi ndi chakwawo. Kwina sakwawa pokwera chulu. 70

Mutu 19

pe

kw yu

Mutu 19

ts ke

su

kw

ts

sa

ts tsu tsitsi tsiku

tsa

tse

tsuka tsata

71

tso

tsi

tsekula

Uyu ndi mwana wasukulu. Iye amatsuka mano ake tsiku ndi tsiku. Amatsata malamulo asukulu. Iye amapesa tsitsi lake. 72

Mutu 20

th

nde

ya

Mutu 20

mb

do

kwa

th

mb

cho

th tho tha thu thi the thawa

thira

dothi

kwathu

73

theka

Dothi lakwathu ndi lachonde. Akwanu amalima kwathu. Dothi lakwanu ndi lamiyala. Ena akuthira dothi lamiyalali mu galimoto. Iwo afuna kukathira ku malo ena. 74

Mutu 20

re

th to

ya

Mutu 20

mb

th

mb

bi

mb mbo mba mbu mbi mbe mbuzi mberere tambala mbumba

75

lemba

Ziweto zimalira mosiyana. Tambala amalira kuti kokoliriko! Mbuzi imalira kuti me! Mberere imalira kuti mbererere! 76

Mutu 21 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oimira zinthu izi.

Mutu 21 3

Werengani maphatikizo otsatirawa.

dze nzo thu kwa tsi 4 2

Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu bokosi ili.

mw ts v th kw nz mb dz 77

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

nzi mwe vi mba tso tse mbu

mbi

kwe

tha

vu nza kwi dzo

dza mwa the va

mbe mwi

Werengani mawu otsatirawa.

vula

dzana

mwake

mudzi

mwano

zunza

theka

kwina

mbombo

tsitsi

dothi

tsekula

78

Mutu 21 5

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Pezani mawu ena omwe ali ndi mw nz kw ts th mb.

Chitsanzo: mw: mwana

1 2 3 4 5 6

mwendo

nz: nzama_____ kw: kwawa _____ ts: tsamba_____ th: thumba _____ mb: mbewa _____

Werengani ziganizo zotsatirazi.

Lero mwezi wawala. Veronika akuvina kwawo. Amama atereka nzama pamoto. Atate amakonda nzama ndi mbatata. 79

Mutu 21 7

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Ikani mwala, mbewa, mwendo, kwathu, thumba kapena nzeru mu mipata ili mu ziganizo zotsatirazi.

Chitsanzo Mwana waima pa _______. Mwana waima pa mwala. 1 ________ wake watupa. 2 Mwana uyu ndi wa ________. 3 ________ kuli mbuzi. 4 Chisomo wasenza _____ laufa. 5 Ine ndikufuna ________ lero.

80

kh

Mutu 22

su

nda

Mutu 22

ng nde

kh

ng

tsa

kh khu kha kho khi khe khasu

khala

khonde

khuta

81

khoma

Awa ndi makolo athu. Iwo akhala pakhonde. Makolowa atsamira khoma. Mwana wakhanda akulira. Iye sanakhute pamene amayamwa. 82

Mutu 22

lo

kh

te

tsa

Mutu 22

ng wo

kh

ng

yi

ng ngi ngu nga ngo nge ngolo

nguli

maungu

anga

83

tenga

Makolo analima maungu ambiri. Maungu ali pa mulu waukulu. Ngolo ikututa maunguwo. Amayi anga atereka maungu okoma. Iwo atenga maungu ndi kupatsa ana. 84

Mutu 23

ns

mp

Mutu 23

ns

mp

nga mbe fe mba

ns nsi nsa nsu nse nso nsalu

nsima

ifenso

nsomba

85

nsembe

Amayi atenga nsima ndi ndiwo. Ndiwo zake ndi nsomba zouma. Ana ambiri amakonda nsomba. Ifenso timakonda nsomba. Nsomba ndi ndiwo zokoma. 86

Mutu 23

nga

ns thu

Mutu 23

mp pi

ru

ns

mp

fu

mp mpu mpe mpa mpi mpo mpunga mpiru mpopi mpeni mpani

87

Amayi akhala pampando. Iwo atenga mpeni waukulu. Iwo akudula masamba ampiru. Mpunga umakoma ndi mpiru. Mpiru ndi wofunika pa thanzi lathu. 88

Mutu 24

nj

nga

Mutu 24

ny

kwe

ri

nj

ny

ha

nj njo

nju

nji

nje

njinga

njuchi

njuta

njenjemera 89

njira

nja

Yohane anakwera njinga yakapalasa. Iye anaona agogo awiri panjira. Anatsika njinga ndi kunjuta pambali. Amuna amanjuta popereka ulemu. 90

Mutu 24

nj

ny

Mutu 24

nj

ny

dzi kha thu mba nja

ny nyu nye nya nyo nyi nyerere nyemba

sonyeza nyanja

91

tinyadire

Izi ndi nyerere. Nyerere zimayenda limodzi. Izo zimasonyeza umodzi wawo. Ife tikhale ngati nyerere. Tiyeni tinyadire umodzi wathu ngati nyerere. 92

Mutu 25

bw

Mutu 25

mt

kwa tsa tha nso

bw

mt

mpi

bw bwi

bwa

bwe

bwato bweretsa

zabwino

bwera bweza

bwereka

93

Onani bwato. Bwato ili ndi lobwereka. Bwali anaona kuti bwatolo ndi labwino. Bwampini amathandiza nawo kupalasa bwato. Pobwera abweretsa nsomba zabwino. 94

Mutu 25

bw

mt

Mutu 25

bw

mt

ngo ndo mbi nso bwi

mt mti mta mtu mte mto mtambo

mtengo

mtolo

mtundu

95

mtondo

Mtengo waukulu ndi wabwino. Mtengo umenewu umabereka zipatso zambiri. Ife timasema mtondo. Ena amathanso kusema ziboliboli. 96

Mutu 26 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oimira zinthu izi.

Mutu 26 3

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani maphatikizo otsatirawa.

nsa

ngo

khe nsu mtu bwi nyi nji njo 4 2

Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu bokosi ili.

ns ny kh mt bw mp nj ng 97

mte

khi

mpe ngu

mpo nje

ngi nya mpa mto bwe nga

kha bwa nse nyu

Werengani mawu otsatirawa.

mpiru

khasu

nguli

tenga

nsomba

khonde

njuta

bwato

mtolo

bwereka sonyeza nyanja 98

Mutu 26 5

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Lembani mayina a zinthu zotsatirazi mu makope mwanu.

Chitsanzo njinga

1

_____

2

_____

3

_____

99

Mutu 26 6

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani ndime yotsatirayi.

Atate ali pabwato. Iwo akuwedza nsomba. Kunyumba amayi akhala pansi pa mtengo. Atereka mpunga kudikira nsomba. Atate afika ndi dengu la nsomba monyadira.

100

Mutu 27

nzi

ph so

nse

Mutu 27

ng’ chi

ph

ng’

ri

ph phi phu pho phe pha phiri

phala

phika

ophunzira

101

phokoso

Iyi ndi sukulu. Ili pafupi ndi phiri. Ophunzira onse amamwa phala. Ophunzira ambiri sakonda kuchita phokoso polandira phala. Phalalo amaphika ndi makolo. 102

Mutu 27

ph

ng’

Mutu 27

ph

ng’

dzi mbe nja nse dzu fu

ng’ ng’u

ng’a

ng’o

ng’ona ng’ombe ng’oma ng’ung’udza ng’anima

103

Onani ng’ombe ndi ng’ona Ng’ombe ili ndi ludzu. Iyo ikumwa madzi. Ng’ona ili ndi njala. Iyo ifuna kuluma ng’ombe. Ng’ombe siikudziwa kalikonse. 104

Mutu 28

nze

dw kha

Mutu 28

ps mbo

dw

ps

yu

dw dwe dwala khalidwe

dwa

dwi

dwazika thedwa

105

chidwi

Abambo awa akudwala. Iwo akudwalira ku chipatala. Adokotala ali ndi chidwi ndi wodwalayo. Atate akudwazika wodwalayo. Iwo athedwa nzeru ndi matendawa. 106

Mutu 28

dw

ps

Mutu 28

dw

ps

bwi nye nja mbi phi

ps pso psu psa psi pse pseda

opsa

psiti

yapsa

pserera

psereza

107

Amayi aphika nyama yambuzi. Nyamayo yapsa bwino kwambiri. Dzulo mwana adapsereza nyemba. Ndiwo zopserera sizikoma konse. 108

Mutu 29

bz

Mutu 29

fw

bz

fw

ngi mbe tsa nso nga

bz bza

bzu

bzo

bzala

bzikula

kubzola

bzalani

109

bze

Alimi amabzala mbewu zosiyanasiyana. Ife kwathu timabzala chimanga. Chimanga chiyenera kubzalidwa motsatira malangizo. Si bwino kubzola mulingo wa kabzalidwe ka chimanga. 110

Mutu 29

tha

bz bza

fw mba

Mutu 29

bz

fw

dzi

fw fwi

fwa

fwe

fwafwaza

fwikofwiko

fwamba

wachifwamba

fwifwa 111

Amayi afwafwaza ndiwo. Afwafwaza ndiwo zamasamba. Iwo akuyanika ndiwo zofwafwazazo. Mwadzidzidzi aona abambo achilendo. Iwo aganiza kuti ndi wachifwamba. 112

Mutu 30

ml

gw

ngo

chu

mte

Mutu 30

de

gw

ml

fa

gw gwe

gwa

gwi

gwada

gwedeza

gwera

gwafa

113

gwira

Onani mtengo wagwafa. Ana agwira mtengo wagwafa. Iwo agwedeza mtengo wagwafa. Gwafa ochuluka wagwa pansi. Ena agwada kuti atole gwafa. Gwafa amakoma kwambiri. 114

Mutu 30

phi

gw nyu

kwa

ml gu

Mutu 30

gw

ml

zu

ml mli mla mle mlu mlo mlamba

mlimi

mlomo

mlendo

115

mluzu

Mlimi akuchokera kudimba. Iye akuimba mluzu mosangalala. Mlimiyu wagula mlamba waukulu. Akufuna akaphike mlambawo kunyumba kwake. Mlamba umakoma kwambiri. 116

Mutu 31 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oimira zinthu izi.

Mutu 31 3

Werengani maphatikizo otsatirawa.

dwe psu ng’o pho ng’e pha gwa bzo fwi

phe dwi mla

ng’a psi gwe

mli fwe

gwi bze

bzu ng’i

fwa dwi 4 2

Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu bokosi ili.

ng’ ml dw gw bz ph fw ps o

117

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

pse mlo

Werengani mawu otsatirawa.

phika

ng’ombe thedwa

ng’anima dwazika

phokoso

bzala

fwamba

gwira

kubzola

bzukula

mlendo

118

Mutu 31 5

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani ndime yotsatirayi.

Mlimi amabzala mbewu zambiri. Amabzala gwafa ndi ndiwo zamasamba. Ndiwo zamasamba amafwafwaza. Mlimi amasunganso ng’ombe. Masiku ena amapha ng’ombe kuti akagulitse. Akagulitsa, amapeza ndalama zothandizira banja lake.

119

Mutu 31

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

6 Tsirizani ziganizo zotsatirazi ndi mawu awa: phala, wafwafwaza, ng’oma, mlimi, apseda kapena abzala.

Chitsanzo Atate ______ pabwalo. Yankho: Atate apseda pabwalo. 1 2 3 4 5

Iye ___________ ndiwo. Amayi aphika ___________. Chikondi akuyimba ________. A Ngozo ndi____ wachimanga. Iwo ___________ mitengo.

120

Mutu 32

mv

Mutu 32

dy

mv

dy

gwa ngu kwa mte nsi

mv mve

mvi

mva

mvula

mvunguti

mvano

imvi

121

mvu mvera

Agogo anga ali ndi imvi zambiri. Iwo aona mtambo wamvula. Mvula igwa posachedwapa. Agogo asekerera mvula ikagwa. Ana omvera amabisala mu nyumba mvula ikamagwa. 122

Mutu 32

mv

dy

Mutu 32

mv

dy

kha dzi nya mpu pha

dy dyo

dye

dya

adya

dyera

mudyo

dyokodyoko

123

chakudya

Banja la a Bengo limakhala pa Dyereni. Banjali limadyera pamodzi. Lero adya nyama ndi mpunga. Chakudyachi ndi chopatsa mudyo. Aliyense kukhosi kuli dyokodyoko kufuna kudya. Amayi adyetsa kaye mwana phala. Onse adikira amayi kuti adyere limodzi. 124

Mutu 33

dya

ms thu

sw dye

Mutu 33

ms

sw

nja

ms msi msu msa mse mso msale

msewu

msika

msirikali

125

msomali

Amayi ali kumsika. Iwo akukagula tomato. Atate nawo apita kumsika. Iwo afuna kukagula msomali. Msikawu uli pafupi ndi msewu. Ana asukulu amagula zakudya zawo pamsika. Tonse timagulanso zofuna zathu kumsika. 126

Mutu 33

ms

gwa

Mutu 33

sw

mbi

yo

swa

swi

ms

sw

mse

sw swe sweka

swera

swiswiri

swana

127

Swiswiri adaswera mu mbiya. Gwaza adagenda swiswiriyo ndi tiana take. Iye mwangozi adaswa mbiyayo. Swiswiri adathawa. Ogo! mbiya ija yasweka. Iye adadandaula. 128

Mutu 34

mk

Mutu 34

mz

mk

mz

mwe dza dzi kwa nga

mk mku

mko

mke

mkaka

mkeka

mkono

mkangano 129

mka mkanda

Atate ndi amayi akuluka mkeka. Mkekawu akuluka ndi milaza yaitali. Mkono umodzi wa atate aupinda pokoka mlaza. Pakati pa atate ndi amayiwa palibe mkangano. Pambali pawo pali botolo lamkaka womwe amwe akamva njala. 130

Mutu 34

mk

mz

Mutu 34

mk

mz

nju nze mba dwa ngo

mz mze mza mzi mzu mzere

mzati

mzimu

mzungu

mzime

Mzuzu

131

Uwu ndi mzere waukulu wa mbatata. Mzerewu adalima ndi mzime wa kwathu. Iye amakhala mu mzinda wa Mzuzu. Mbatatayi adzaigulitsa ku Mzuzu komweko. Ndalamazo adzagulira mzati wa nyumba. 132

Mutu 35 1

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Tchulani liwu loyamba mu mawu oimira zinthu izi.

Mutu 35 3

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani maphatikizo otsatirawa.

mve mzi swa

mku msi 4 2

Tchulani maliwu a malembo kuchokera mu bokosi ili.

mso dye bzo

swe mva mko

mza mvi

dya msa

Werengani mawu otsatirawa.

imvi

dyera

mv sw ms

mkono

mvula

sweka

mkeka

mz dy mk

msale

msika

o

133

134

Mutu 35 5

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

Werengani ndime yotsatirayi.

Msirikali wina wakhala pa mkeka. Iye akudya chakudya chopatsa mudyo. Pambali pake pali mbiya. Mu mbiyamo muli mkaka. Iye amwa mkakawo akamaliza kudya chakudya chake. Msirikaliyo aona mtambo wamvula. Iye anena, “Mvula igwa posachedwa.” Pothawa mvula aswa mbiya ija.

Mutu 35

Kubwereza ndi kuyesa ophunzira

6 Sankhani mawu oyenera kuchokera mu mawu omwe mwapatsidwa.

Chitsanzo Agogo aona mtambo wa ______. (madzi, imvi, mvula) Yankho: Agogo aona mtambo wa mvula. 1 Amayi _______ mwana phala. (adyetsa, alemba, aseka) 2 Yohane akukagula ______ ku msika. (msale, imvi, mzungu) 3 Atate akuluka ________. (khasu, mkeka, msewu) 4 Mbiya ya agogo ya ________. (sweka, yenda, dyera)

135

136